Chichewa:
Heaven is so Real
by Choo Thomas
translation help by Francis Mendulo

munthu wa Chikorea wa ku America dzina lake Choo Thomas,
wakhala obadwa mwatsopano. Chimene chikupangitsa nkhaniyi kukhala ya padera
ndi choti patatha zaka ziwiri chitembenukire,
Choo anachezeredwa ndi Yesu Khristu wa Ku Nazarete.
Anakhala akuperekezedwa kumwamba nthawi zambiri ndi kuonetsedwa Hade kawiri.
Choo Thomas walemba buku la zomwe iye anakumana nazo;
bukuli limatchedwa “Kumwamba kulipodi” ndipo linatsindikidwa mu Okotobala 2003.
Mchaka chimodzi chakutsindikizidwa,
bukuli lakhala logulitsidwa kwambiri padziko lonse la pansi
komanso lakhala mgulu la mabuku apamwamba khumi a Chikhristu ku America.
Zitheka bwanji mzimayi wapakhomo, amene amalakhula Chingerezi chosakwanira,
osati kungokwanitsa kutsindikiza buku, koma mkati mwa chaka chimodzi chakutsindikizidwa,
kukhala buku logulitsidwa kwambiri padziko lonse lapansi?
Kapena funso lofunikira kwambiri ndiloti
chifukwa chiyani mabvumbulutso awa tsopano.
“Kumwamba kulipodi” ndipo iyi ndi nkhani ya Choo Thomas.
Atate wa Kumwamba, zikomo pondilola ine kuti ndichitire umboni. Aleluya!
Ndakhala ndili Mkhristu kuyambira chaka cha 1992
ndipo ndinagwa muchikondi ndi Yesu nditapita kutchalichi kanthawi kochepa
ndipo ndimafuna kupereka gawo lina liri lonse lamoyo wanga kwanthawi yonse.
Ndikufuna ndiyankhule mwachidule za buku lotchedwa “Kumwamba Kulipodi”.
Ambuye Yesu ananditengera ku mwamba
kakhumi ndi kasanu ndi kawiri thupi langa liri losandulizidwa,
ngati momwe ndinali ndi zaka 15 kapena 16 zakubadwa.
zisanachitike izi, Anandikonzekeretsa mu zonse mwatsatane tsatane.
1994 Anandidzodza thupi langa lonse ndi Moto, kenaka patatha mwezi umodzi,
Anaonekera kwa ine ndi thupi looneka ndikulambira ku tchalitchi.
Ndipo mu 1995, La Mulungu la Ambuye, Anandidzodza ndi thupi lonjenjemera
kuyambira pomwepo, thupi langa limanjenjemera kutchalitchi ndinthawi yanga yamapemphero.
Mukuona, thupi langa likuyenda mopita kutsogolo ndi kumbuyo,
ngati sindichita izi, mimba yanga ikhala yomangika
ndipo imakhala ngati iphulika; ndichifukwa chake ndikuyenda mopita kutsogolo ndi kumbuyo.
Choncho chonde musanganize kena kalikonse kolakwika ndi thupi langa.
Ndi Mzimu Woyera akuchita izi, chifukwa ndikukamba za Yesu.
Ndipo patatha izi, Anandibatiza ndi Mzimu Woyera,
ndikuyankhula ndi malirime atsopano, nyimbo zakumwamba ndi kuseka muuzimu.
ndipo ndinazozedwa kwambiri, kwa maola atatu ndinali ndili pansi,
sindikanatha kudzuka chifukwa zinali zamphamvu kwambiri.
Zitatha izi, miyezi yochepa itadutsa, Abusa Larry Randolf, ananenera pa ine
kuti Mulungu akufuna atandigwiritsa ntchito mwapadera-dera.
Ndipo uneneri wake wonse wakwaniritsidwa, kwambiri, mwina kuposa apo.
Zitatha izi, mu Januale 1996, Ambuye Yesu,
Amandiyendera ndi kupezeka kwa masomphenya.
Anandichezera kakhumi ndikundiuza mmene adzandigwiritsire ntchito,
ndi mapulani ake, Amandiuza kuti, monga ziliri m’bukumu.
Koma sanandiuze kuti adzanditengera kumwamba.
Choncho, kanthawi kokwanira ka khumi, pa Febuluwale 19, 1996,
Anayamba kunditengera kumwamba ndi thupi langa losandulizika,
monga Thupi lake lauzimu, chomwechonso thupi langa.
Nthawi ina ili yonse asananditengere kumwamba, Ananditengera mbali mwa nyanja, nyanja yapadziko lapansi.
Nthawi yoyambirira asananditengere kumwamba,
Ananditengera ku mbali ina ya gombe la nyanja ndipo anandionetsa madzi omwe amaoneka oyera kwambiri
kenaka Iye anandionetsa mphanga yowala yaikulu. Ndipo kenaka ananditengera kumwamba.
“Atatha kudutsa mumphangayo, Choo akulemba kuti:
“Ambuye ndi Ine tinayenda mbali mwa nsewu omwe umachokera pa mwamba pa phiri.
Mapeto ake tinakafika pa chipata chachikulu choyera kutsogolo kwa chinyumba chachikulu choyera.
Tinadutsa pa chipata ndikupitirira kulowera ku chinyumba choyera.
Tinalowa ndi kuyenda kulowera ku chipinda chachikulu.
Chomwe tinalowa. Nditayang’ana pansi, ndinazindikira kwa nthawi yoyamba
kuti ndinali nditavala mkanjo wosiyana ndi omwe ndinavala pamene ndinali pa gombe,
ndipo ndimamva china chake cholemera pamutu panga.
Nditagwira ndinazindikira kolona wokongola anali atayikidwa popanda kuzindikira kwanga.
Kenaka ndinayang’ana Ambuye mwachindunji.
Anali atakhala pa mpando, ndipo anavala chobvala chowala ndi kolona wa golide.
Ena anali pamenepo ndi ine, atagwada pansi ndi kugona chafufumimba pamaso pa Iye.
Makoma a chipinda anali opangidwa ndi miyala yayikulu koma yowala
ndipo mitundu yosina siyana ya miyala imapanga maoenekedwe a chipindacho kukhala
ooneka ofunda ndi okondweretsa, komanso opatsa chidwi.
Kenaka, monga mmene ndinayendera kupita pa phiri
ndikulowa mchinyumba choyera, ndinazipeza ndekha ndiri pa gombe.
Nthawi yoyamba, Anangondionetsa chipinda chake cha Ufumu.
Kenaka zitatha izi tinatsika kuchoka kumwamba
ndipo tinakhala pa mchenga wapagombe la nyanja.
Ndipo anayamba kulakhula. Anati, tangopita ku Ufumu wa Kumwamba.
Okhawo amene adzabwere kumeneko ndi omvera ndi amgwiro mumtima
ndipo anati “Kulalikira uthenga ndi chinthu chofunika kwambiri” ndipo anadikira pang’ono.
Anati, “iwo amene sapereka chakhumi ndi Akhristu osamvera.”
Ichi chinali chinthu chomaliza Iye ananena pa ulendo oyamba.
Choo anapita kumwamba kanthawi kenanso kokwanira kakhumi ndi kasanu ndi kamodzi, mukupita kulikonse, akulemba:
Mu thupi langa losandulizika, Ine ndinayenda ndi Ambuye pa gombe,
ndipo kenaka anandiperekeza kumwamba.
Tinayenda kudutsa mu zipata zowala ndikupita ku chinyumba choyera kukasintha zobvala zathu.
Titasintha, tinayenda kudutsa mlatho wagolide.
Izi zimaoneka zosadabwitsa kwa ine.
Okhulupirira aliyense, ndikhulupirira, adzadutsa momwemo pamene apita kumwamba.
Patatha izi, Iye ananditengera kumwamba kakhumi ndi kasanu ndikamodzi.
Nthawi ina iliyonse ananditengera kumeneko, anandionetsa zinthu zosiyana-siyana.
Ndipo pamene anandionetsa zinthu zapadera,
Amanena nthawi zonse kuti, “Ndinakozera izi ana anga, ndimadziwa zimene amakonda.”
Monga pamene anandionetsa gombe, “ukuona mwana wanga m’mene gombeli kukongola kwake,
Ndikudziwa ana anga amakonda gombeli” ndipo ananditenga kukapha nsomba,
“Ndikudziwa ana anga amakonda kupha nsomba”,
“ndichifukwa chake ndimakonza zinthu zambiri monga mmene amakondera.”
ndipo ndinazindikira kuti kumwamba ndikokongola kuposa dziko la pansi koposa ka zikwi zikwi,
koma pali zinthu zambiri monga pa dziko lapansi, monga misewu, nyumba, mitengo.
thengo, miyala, maluwa, ndi malo ovuta kunja kwa ufumu;
kuli zinthu zambiri kumeneko;
koma ndizokongola ka chikwi koposa zinthu za dziko lapansi, zokongola wamba.
Kukongola kwa kumwamba ndikosafotokozereka, sindingathe ngakhale kufotokoza
mmene kukongola kwake kuliri, ndizokongola
Ndikuzindikira mmene Yesu amakondera wina aliyense wa ife.
Mmene anayankhulira ndi ine kunali ngati kunena kuti
“ukuona mmene ndimakondera ana anga ndipo ndinawachitira zinthu zonsezi.”
Ichi ndichifukwa ananditengera kumeneko kukandionetsa zimene wakonzera ana ake,
kotero aliyense adziwe zimene zikutiyembekezera kumwamba,
choncho Iye asanabwere, akufuna Akhristu onse adziwe zinthu izi,
kuti akhale osangalala ndi kupita kumeneko.
Ichi ndichifukwa ndikukhulupirira anandionetsa zinthu zimenezi.
Samandiuza zili zonse.
Amangondionetsa zinthu zina,
Amanena zinthu zochepa, zofunika mau.
Umu ndimene Mulungu alili. Mulemekezeke Ambuye.
Kupatula zomwe anakaona kumwamba, Choo anakaonetsedwanso ku Hade.
Pa izi akulemba:
Ndimaona nthuzi ndi mtambo wakuda ukukwera kuchokera ku dzenje lakuya.
Zimakhala ngati chiphala chamoto chochokera mphiri
ndipo mkati ndimaona Malawi a moto akuotcha unyinji wambiri wa anthu omwe anali kukuwa
ndi kulira monga kubuula omwe okhawo okupsya kwambiri angadziwe.
Anthuwo anali maliseche, opanda tsitsi, ndipo atayima pafupi wina ndi mnzake,
akuyenda ngati mphutsi, ndipo Malawi a moto amaotcha matupi awo.
Panalibe kuthawa kwa iwo amene anali ogwidwa muzenje-makoma ake anali
okuya kwambiri kuti iwo angakwere, ndipo makala amoto anali ozungulira mbali mwake.
Ngakhale Ambuye sanandiuze za izi,
Ndinadziwa kuti ndaima mbali mwa hade.
Kumwamba china chilichonse chomwe anandionetsa chinali chosangalatsa ndichodabwitsa
koma kenako, anandionetsa hade. Ananditengera ku hade,
chinthu choyamba chomwe ndinaona mkati mwake chinali moto wokhawokha, zenje lakuya, lakuda, lopanda malire.
Anthu anali amaliseche ndi opanda tsitsi.
Analibe tsitsi, analibe zobvala, anali ndi matupi amaliseche.
Anayima moyandikana wina ndi mzake.
Zimaoneka ngati amakakhana wina ndi mnzake chifukwa amafuna
kuti atuluke mmoto. Nthawi ina iliyonse amasuntha, moto umawalodola,
kutsogolo ndi kumbuyo, kutsogolo ndi kumbuyo, malo onsewo anali ndi moto,
anthuwa amaima pafupi wina ndi mnzake.
Anali muululu komanso osakondwa, ndinayamba kuwalirira.
Ananditengerako kachiwiri ndipo ndinaonanso anthu omwewo.
Ndipo ndinamva mau ndipo ndinayang’ana mbali imeneyo, kunali anthu ambiri kumeneko.
Ndipo mzimayi mmodzi uyu, ananditukulira dzanja, nati “Kutetha, kuthentha kwambiri!”
Ndinayang’ana pa iye ndipo maso athu anakumana. Anali mai anga!
Pamene ndinazindikira kuti anali mai anga, mtima wanga unasweka ndipo ndinayamba kulira.
Sindinamvepo kuwawa kotero, kuwawa.
Kuwawa kwambiri, sindinadziwe choti ndingachite.
Ndipo anapitirira kunena “kutentha, kutentha” uku akukupiza nkono pa ine.
Ndipo m’mene ndinaonera, amafuna ine ndiwathandize.
Kenako ndiyang’ana pa anthu ena, kunali bambo anga,
mai anga ondipeza, dzakhali wanga wang’ono, anafa ali wang’ono
ndi amnzanga omwe ndimawadziwa.
Oh, kunali kukumbukira kowawa ndipo ndimalira, kulira, kulira,
ndipo Ambuye Yesu anati kwa ine “mwana wanga, ndili ndi zifukwa zabwino pokuwonetsera izi,”
“koma ndikumva kuwawa koposa mmene iwe ukumvera”.
Uumm. Ndinati, Ambuye, mai anga, anafa ali aang’ono, anadwala nthawi yayitali.
sindikukhulupirira kuti anali munthu woipa.
Iye anati, zilibe kanthu kuti anthu ndi abwino motani,
wina aliyense amene sandidziwa Ine, awa ndi malo amene ayenera kupita.
Koma mu mtima mwanga ndimati, “Chifukwa chiyani mukundionetsa izi, ndikundipweteketsa mtima chonchi?”
ndimaganiza zonena choncho, koma sindikanamkwiyira Iye.
Sindinathe kuona nkhope yake, koma ndinatha kudziwa kuti amalira nane limodzi.
Ndinamva choncho. Amaoneka okhumudwa, kenako anakhudza mutu wanga, anagwira dzanja langa,
tinayenda kutuluka kumeneko ndipo ndimalira nthawi yonse imene timayenda.
Chabwino, mbuku langa, ndinafotokoza zinthu zonse,
choncho, kenako, ulendo wachiwiri anandionetsanso chinthu china chokhumudwitsa.
Chinali ana ophedwa pochotsa mimba. Ananditengera ku malo amodzi awa, inali nyumba yaikulu.
Imaoneka ngati nyumba yosungiramo katundu. Titalowa mkati, chomwe ndinaona chinali ana,
tating’ono, tating’ono tamaliseche. Ndipo anagona pafupi -pafupi.
Humm, ndipo ndinayamba kulira. “Ambuye, chifukwa chiyani ana ambiri?”
Anati, “Ndi ana omwe anafa pochotsa mimba.” Ndinati, “Ndiye muchita nawo chiyani amenewa?”
Anati ngati mai awo adzapulumutsidwa ndikubwera kumwamba,
adzakhala nawo ana awo.
Paulendo wawo wa kakhumi ndi kasanu ndi kawiri, Yesu anaumuuza Choo kuti uwu ukhala ulendo wake omaliza.
Pa izi analemba kuti: Mau ake anandikhudza kwambiri.
Mtima wanga unawawa ndi chikondi cha Ambuye wanga.
Anayimirira, ndipo ndinadziwa kuti inali nthawi yoti tisiyane. Ndinapitirira kulira,
koma mtima wanga unatsimikizika kuti ndikakhala ndi Ambuye kwa nthawi yonse
ndikuti adzakhala ndi ine nthawi zonse pa dziko lapansi.
Kumalo obvalira, mngelo wa Ambuye anandikumbatira.
Zinali zabwino kukhala pa malo amene anali ndi chikondi chambiri,
chisoni ndi kumvetsetsa zinali zopezeka.
Pamene ndimasintha chobvala changa, ndinadabwa kuti onse Abrahamu ndi
mngelo anadziwa kuti uwu ndi ulendo wanga omaliza kupita kumwamba.
Pamene ndinatuluka mu chipinda chobvalira, mngelo anandikumbatira kamodzinso.
Mngelo uyu anali ndi tsitsi lalitali, mkanjo wautali ndi nkhope yachimwemwe.
Mngelo anandimwetulira pamene ndimayenda kulowera komwe kunali Ambuye.
Pamene Ambuye Yesu ananditengera kumwamba ulendo omaliza, anandionetsa mitambo.
Uku kunali kumaliza kwa maulendo anga a kumwamba.
Ambuye anandiuza kuti uwu unali ulendo wanga omaliza opezeka kuno.
Sindizakubweretsanso kuno mpakana tsiku lomaliza.
Ndinamva kuti ndinadziwa izi, kuti linali tsiku lomaliza.
Ndipo ndinayamba kulira, chifukwa sindimafuna kuchoka kumeneko.
Ndimagwira dzanja lake ndipo ndinati Ambuye, chonde ndisapite,
sindikufuna kupita chifukwa ndikufuna kumabwera kuno kawiri kawiri.
Chinali chinthu chomvetsa chisoni kwambiri, kuti sindizapitanso kumeneko
chifukwa nthawi ina ili yonse ndimapita ndi Iye kumwamba, ndimaona zinthu zokhumudwitsa,
koma chimwemwe, mtendere, sindingathe kufotokoza, sindingathe kufotokoza chimwemwe, mtendere umene ndimakhala nawo ndi Iye
Ngakhale okhumudwa, ndinali ndi chimwemwe, mtendere.
Chikondi chachikulu, ndinalira masiku ambiri zitatha izi.
Baibulo limanena za tsiku limene Yesu Khristu adzabwera kubwerera Mpingo wake.
Ku 1 Atesalonika 4:16, akuti, “Pakuti Ambuye mwini wake adzabwera kuchokera kumwamba”,
“ndi mfuu, ndi mau a mngelo wamkulu”
ndi lipenga la Mulungu; ndipo akufa mwa Ambuye adzayamba kuuka;
“pamenepo ife okhala ndi moyo, otsalafe”
“tidzakwatulidwa nawo pamodzi m’mitambo”
“kukakomana ndi Ambuye mlengalenga, ndipo potero tidzakhala ndi Ambuye nthawi zonse”.
Ichi chimadziwika ngati “Mkwatulo”.
Patatha izi zonse, masabata otsatila, Ambuye Yesu,
Anandibweretsa ine ku gombe ndi thupi langa lauzimu.
Ndipo tinakhala pamalo omwe timakhala nthawi zambiri, ndipo tinayankhula kanthawi
Anandiuza kuti, ndikuonetsera chinthu china.
Nthawi yomwe ananena izi, ndinakhala ndi masomphenya.
Nthawi ina ili yonse anandionetsa chinthu chapadera, ndimakhala ndi mau a masomphenya
iwo amene amachokera mkati mwa thupi langa, mmimba mwanga.
Anali omveka ndipo masomphenya anatenga nthawi yayitali.
Kenaka ndimamva phokoso, mau okwera,
Ndimamva ngati dziko lonse likugwa, phokoso loopsya, komanso lomveka mokwera.
Nditayang’ana, mpweya onse unali mbee.
Anthu obvala mikanjo yoyera akuuluka pena pali ponse, akumangotuluka,
kutuluka, kumasowa ndi kumatuluka. Mlengalenga unadzadza ndi anthu.
Ndipo ndinadziwa kuti uku kunali kukwatulidwa.
Ndimaseka, kulira, kukuwa, osangalala,
ndipo pamene ndinaona mdzukulu wanga wamkazi, ali ndi miyezi khumi yokha, alibe tsitsi,
mwadzidzidzi anauluka kutulukira pa zenera.
Kenaka ndi mkanjo woyera tsitsi lake linamera mpakana mapewa.
Mungathe kuganize za mmene ndinakondwera.
Ndipo mphindi yotsatira, ndinaona mdzukulu wanga wina wamkazi,
anali ndi miyezi inayi yokha, alibenso tsitsi.
Anauluka kutuluka pa zenera, monga mmene anachitira wina, ndi mkanjo woyera.
Ndipo tsitsi lake linabweranso mpaka mmapewa.
Ndimakuwa, kulira, kuseka, kukondwera.
Sindinakondwepo motero chiyambire, kungokondwa. Nyumba imamva.
Umbwino wake mwamuna wanga kunalibe.
Akanakhala kuti anali pakhomo, akanaganiza kuti china chake chinalakwika ndi ine.
Zitatha izi, Mulungu anandionetsera zinthu zina.
Chinthu ichi chinali chokhumudwitsa. Chinali choopsya.
Baibulo limakambanso za nthawi yowawitsa, patangopita mkwatulo.
Mu Mateyu 24:21-22, Yesu anati “pakuti pomwepo padzakhala masauko akuulu”,
“monga sipadakhale otero kuyambira chiyambi cha dziko, kufikira tsopano, inde ndipo sipadzakhalanso.”
Ndipo akadaleka kufupikitsidwa masiku awo, sakadapulumuka munthu aliyense:”
“koma chifukwa cha osankhidwawo masiku awo adzafupikitsidwa.”
Ichi chikudziwika ngati “Chizunzo chachikulu”.
Chabwino, patatha izi, Ambuye Yesu anandionetsa masopmphenya ena.
Ichi chinali anthu omwe anasiyidwa. Ndikhulupirira mkati mwawo munali Akhristu ambiri.
Nchifukwa chake anali kuthawa.
Ngati sanali Akhristu, sibwenzi atathawa.
Apolisi anali paliponse, anthu anali pali ponse ndipo
anali kuthawa mwa mantha, mwampani mpani, kupita kugalimoto,
kupita kubwato, kuthamangira kumapiri,
samadziwa koti angathe kupita,
monga ngati kuti amathamangitsidwa ndi chilombo kapena china chake.
Anali amantha. Chinali chinthu choopsya kwambiri.
Ndipo zitatha izi, Ambuye Yesu anati,
Anandiuza kuti zimene wangoona kumene ndi chabe kuyerekeza ndi zimene zizachitike pamene tsikulo lidzafika.
Ndipo zitatha izi anandiuza kuti, anthu anga onse akadzakwatulidwa, Satana adzakhala ndi mphamvu padziko
ndipo adzafuna wina aliyense kuti alandire nambala ya 666.
Ndipo aliyense wokana kulandira, adzadulidwa mutu.
Choncho wina aliyense wosafuna kulandira chizindikiro cha chilombo nambala 666,
amapereka mtima wawo kwa Yesu, akufuna kukhala ndi Iye kwanthawi zonse, Chibvumbulutso 20:4
Ndipo kenaka, wina aliyense olandira chizindikiro cha chilombo nambala 666,
onsewo adzaponyedwa mu nyanja ya moto kwamuyaya,
adzakhala akupsya kumeneko usana ndi usiku, osapuma, Chibvumbulutso 14:11
Choncho wina aliyense ayenera adziwe zinthu izi
ndi kukumbukira, ngati mukufuna kudulidwa mutu, sizidzakhala zophweka.
Adzazunzidwa kwambiri asanadulidwe mutu,
chifukwa satana sadzawalola kungowasiya.
Ndiye, aliyense wakumva uthenga uwu,
chonde, ngati mulibe ubale wozama ndi Ambuye wathu Yesu,
chonde chitanipo china chake cha chipulumutso chanu.
komanso, ngati mudzasiyidwa, kaya muzakumana ndi zotani,
musazatenge, chizindikiro cha chilombo nambala 666.
Kuli bwino kuvutika kwa ka nthawi koposa kukavutika ku Hade kwamuyaya
kuyaka mmoto. Chonde, chonde tengani zomwe ndikunena motsimikizika.
Bukhu langa, Kumwamba Kulipodi, likumasuliridwa mu dzilankhulo zosiyana-siyana
ndikugawidwa pa dziko lonse lapansi.
Komanso pali buku la pa MP3, Lomwe lingathe kukopedwa pa intaneti.
Chabwino, bukhuli likhuthandiza. Ndipo likugulitsidwa kwambiri padziko lonse.
Ambuye anagwiritsa Dr. Yonggi Cho pabukhu limeneli, analimasulira.
Linamutengera pafupi fupi miyezi iwiri akulimasulira, koma nthawi zambiri limatenga miyezi isanu ndi umodzi, kapena isanu ndi iwiri.
Choncho, tsiku lomwe bukuli linatuluka linafalikira mu Korea ndikukhala buku logulitsidwa kwambiri.
Ndipo Mulungu anagwiritsa ntchito Dr. Yonggi Cho munjira yodabwitsa.
Ali ndi pafupi fupi mamembala 800,000 mu mpingo mwake,
kotero Mulungu akumugwiritsa ntchito pa buku ili, anamusankha pa bukuli.
Ambuye alemekezeke, ndipo bukuli ndi buku lanthawi yomaliza la Ambuye Yesu.
Akufuna kuti Akhristu onse awerenge bukhuli ndi kuchitira umboni kwa ena
izi ndi zimene anthu ambiri akuchita,
akagula bukhuli, akugula ochuluka, akugula makumi khumi,
ndipo akuti ichi ndi chida chabwino chogwiritsa ntchito pochitira umboni pambali pa Baibulo.
Ndipo kenaka, ndikulandira makalata ambiri, ndilibenso nthawi ya ine mwini.
Makamaka ndikalandira makalata ochokera kwa ana anag’ono azaka zokwana khumi ndi ziwiri, khumi ndi zitatu zakubadwa.
Amati akulikonda kwambiri bukhuli.
Amakonda Yesu, amalitchula bukhuli kuti ndi bukhu la Yesu ndipo akusinthika ndi bukhuli.
Ena amati asiye sukulu ndi kugwira ntchito ya Mulungu?
Ndimati “musasiye sukulu.”
Mukuyenera kuphunzira, Mulungu akufuna inu muphunzire. Ndizimene ndimawauza.
Koma mu chili chonse chomwe muchita, ikani Mulungu patsogolo.
Ndikayankha makalata awo, amakondwera,
Mukudziwa, miyoyo yambiri ikusinthika
ndi bukhuli chifukwa ndi bukhu la Yesu.
ndipo anakwaniritsa malonjezano ake a bukhuli kuyambira pa chiyambi mpaka kumapeto.
Anandiuza, asamalira chiri chonse, kuyambira koyambirira mpaka kumapeto.
Ndinamuuza kuti, ndinali odandaula ndi zinthu zambiri,
ndipo anandifunsa, chifukwa chiyani ukudandaula, ili ndi bukhu langa,
ndisamalira chiri chonse, amandiuza choncho nthawi zonse.
Koma wakhala akusamalira kali konse kuyambira koyambirira mpaka kumapeto.
Aliyense amene awerenga bukhuli, amadziwa kuti ili ndi Bukhu la Yesu ndipo anasamalira kali konse.
Choncho, malonjezano ake onse abukhuli, anakwaniritsidwa.
Tsono, chomwe chatsala ndi utumiki wanga wovina.
Anandiphunzitsa utumiki wovina;
uku ndi kuvina koyera, ndinavina kutchalichi kwa zaka ziwiri.
Tsopano pafupi-fupi zaka zitatu ndi theka, ndikudikira.
Kudikira ndi gawo lovutitsitsa lotumikira Mulungu.
Mukudziwa, ndinadikira zaka zisanu ndi ziwiri asanatsindikize bukhuli.
Nthawi zina ndimaganiza, “Kodi adzalitsindikiza?” Koma anakwaniritsa mau ake.
pakutha pa maulendo ake akumwamba, Yesu anapanga lonjezo lapadera kwa Choo Thomas.
Chabwino, mapeto a ulendo anali nditayang’anira ntchito yoyamba yotsindikiza bukhuli.
Kenaka anandibweretsa ku gombe lapadziko lapansi. Ndipo tinakhala ma ola angapo.
Anandiuza kuti azindibweretsa pamenepo Lolemba liri lonse. Panali pa 27 Meyi chaka cha 1996.
Kuyambira pomwepo, sanaphonyepo ngakhale kamodzi,
Amanditengera pamenepo lolemba liri lonse ndi thupi langa losandulizika.
Amandizutsa mphindi zochepa pakangokwana pakati pa usiku m’mawa wa Lolemba liri lonse.
Amagwedeza thupi langa kwa mphindi zokwana makumi atatu, osachepera apo, komanso osapitirira apo,
ndipo kupezeka kwake kumaonekera ndi thupi lake lauzime, thupi langa la uzimu timapita kugombe la nyanja.
Ndipo tikapita kumeneko, mukudziwa, amalankhula kwambiri, ine ndimamvetsera.
Ndipo ndimayimba, ndimavina ndi thupi langa lauzimu
ndipo iyi ndi nthawi yabwino ya moyo wanga tsopano
Molingana ndi malembo, chifukwa chimene Yesu anafera pamtanda ndichifukwa cha Yohane 3:16
“Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi napereka mwana wake wobadwa yekha”
kuti yense wokhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha”.
Kotero, molingana ndi Aroma 10:9 –“Ngati muvomereza ndi mkamwa mwanu, ‘Yesu ndi Ambuye”,
“ndikhulupirira mu mtima mwanu kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, mudzapulumuka”.
Chabwino, ndimamva anthu ambiri akunena “ndani amene amasamala ine ndikazafa?” Hee hee hee, mpaka choncho.
Ndiye ndimati, “Muyenera kusamala mukadzafa.” Izi zinali pamene ndinali kuchitira umboni.
Ngati mutafa, mumapita kumalo awiri, kaya kumwamba kapena ku Hade.
Amati, “eeeehhhh, ndani asamala ndikazafa.”
Amalankhula ngati sakudziwa kali konse akadzafa.
Ndimati, muyenera kusamala mukadzafa, chifukwa?
Ngakhale mukafa, thupi lanu limafa, koma mzimu ndi moyo sizimafa.
Ichi ndi chifukwa mumatha kukumbukira, kuwawa, kukondwa, chimwemwe, chiri chonse, monga mmene munali muli moyo.
Kotero samakhulupirira, aaaaa, amandipsyera mtima.
ndimati, ndikhulupirira tsiku lina muzakumbukira zomwe ndikunenazi.
Mumamudziwa Yesu? Amati, “Ndimamudziwa Mulungu.”
Ndimati, chabwino, Yesu ndi Mulungu. Ndi Tate, Ndi Mzimu Woyera, Ndi zonse.
Ngati simumamudziwa Yesu, inu kumudziwa Mulungu, sizizakutengerani kumwamba.
Ndimangolankhula, kulankhula, samafuna kumva, ambiri a anthu.
Ndimangowuza, chabwino, simufuna kukhulupirira lero, ndikhulupirira tsiku lina, mudzakhulupirira.
Ndipo ndimayankhula, kuyankhula, kaya motani, samafuna kuvomereza phukusi la chipulumutso.
Mukudziwa zimene ndimanena, ndimati, chabwino simukufuna kuvomera phukusi la chipulumutso
koma tsiku lina, mudzadziwa kuti anthu onse a Mulungu adzakwatulidwa,
kenaka mudzadziwa kuti zimene ndimanena zinali zoona,
koma ndikukuuzani, pamene nthawi idzafika, musadzalandire nambala ya 666.
Ngati mudzalandira, mukupita kokapsya ku Hade kwamuyaya.
Choncho, chonde, chonde, musadzalandire nambala ya 666.
Kodi mudzakumbukira? Mukudziwa, ena a iwo amati chabwino.
Ndimanena izi kwa anthu ambiri.
Ngati wina wake sanapempherepo pemphero la chipulumutso, ndingakonde kuti ndipemphere nanu.
Chonde mubwereze pa ine. Ambuye Yesu,
Ndikhulupirira ndinu Mwana wa Mulungu ndipo munandifera ine.
Chonde bwerani mu mtima mwanga ndipo mukhale Mbuye ndi Mpulumutsi.
Ndikufunsani mundikhululukire machimo anga onse
ndi kundiyeretsa ndi mwazi wa mtengo wapatali,
tengani ulamuliro madera onse a moyo wanga kuyambira tsopano.
Yesu, dzadzeni ndi Mzimu Woyera ndipo mundipatse mphamvu kukagwiritsidwa ntchito kuulemerero wanu.
Ndikufuna kukutumikirani, kukukondani, kukumverani masiku onse amoyo wanga
ndikupanga kusintha miyoyo ya anthu ambiri.
Atate, zikomo pondipanga kukhala mmodzi wa ana anu.
Mdzina loyera la Yesu, ameni Haleluya!
Aliyense amene mwapemphera pemphero ili ndi ine,
chonde, pitani ku tchalichi, mverani mau a Mulungu kuchokera kwa Abusa,
kawerengeni Baibulo tsiku liri lonse,
Pempherani nthawi zabiri pa tsiku ndipo mukhale ndi ubale ndi Yesu.
Zikomo, ameni, Aleluya
Mmalo mwa Utumiki wa Choo Thomas zikomo powerenga nkhaniyi
Mu “Kumwamba Kulipodi” Yesu anati akubweranso kubwerera Mpingo wake mwansanga koposa mmene tinganizira,
choncho konzekerani ndipo tiyeni timpatse Mulungu malemekezo onse.